Top Songs By Lucius Banda
Credits
AUSFÜHRENDE KÜNSTLER:INNEN
Lucius Banda
Künstler:in
KOMPOSITION UND LIEDTEXT
Lucius Banda
Komponist:in
Lyrics
Moyo uno anthu Inu ndi ovuta
Pali zokoma pamakhala zowawa
Yamika yemwe agonjetsa zowawa
Mudzasangalala
Moyo uno uli ngati uchi
Pali uchi pamakhalanso njuchi
Kuyamika yemwe mwadziotcha njuchizo
Udzadya malesa
Mukamawalangiza anawa
Musamawabisire zambiri
Poti mwadzidzidzi mwina Inu mudzafa
Adzalira!
Mukamawalangiza anawa
Musamangowauza adzakhala bwana
Poti mwinamwakwe adzakhala antchito
Adzalira!
Mukamamulangiza mwanayo
Mumuwuze m'moyo muli mavuto ndi zokoma
Bread tidye lero mawa chinangwa
Ndiye moyowo!
Moyo wa munthu pali nthawi yokondwa
Komanso dziwa kuti pali nthawi yolira
Ngati sunavutike ukali wang'ono
Thokoza Mulungu
Mukamawalangiza anawa
Musamawabisire zambiri
Poti mwadzidzidzi anzaga mudzafa
Adzalira!
Mukamawalangiza anawa
Musamangowauza adzatola ndalama
Poti mwinamwakwe adzataya ndalama
Adzalira!
Musamale pofuna kuthandiza
Pokuti nzukwa umaoneka monga nzimu
Si onse omwe udzawathandize adzasangalare
Ambuye anati kondani adaniwo
Omwe achenjera poti satana ndi mdaniso
Mukapusa mudzayanjana ndi satana
Mu dzina la Mbuye
Mukamawalangiza anawa
Musamawabisire zambiri
Poti mwinamwake anzanga tidzafa
Adzalira!
Mukamawalangiza anawa
Musamangowauza adzakhala a police
Poti mwinamwakwe adzakhala akayidi
Adzalira!
Mukamawalangiza anawa
Musamawabisire zambiri
Poti mwadzidzidzi mwina Inu mudzafa
Adzalira!
Mukamawalangiza anawa
(Musamangowauza adzakhala a ndalama)
(Poti mwinamwakwe adzataya ndalama)
(Adzalira!)
Lyrics powered by www.musixmatch.com