Top Songs By P. Kay
Credits
KOMPOSITION UND LIEDTEXT
Pilirani Kumasewera
Songwriter:in
Lyrics
Ey, yo
Eko pen, gwira paper
Upeze nthawi uyambe kulemba
Each and every step yomwe umafunitsita utadzayenda
Ma page ndiosayamba utambasule masomphenya
Ndi zokhumba kaya ufuna kukhala bwana kaya venda
Nthawi ndikupatsa
Masiku uchita kutaya ndi maola ankhani-nkhani zili ndi iwe kusankha
Kuikazinga upeze phax yoti udye lelo
Kapena kukaidzala idzakupatse madyelelo
Nena fast, tiyenda bwanji
What's the plan? Za ulesi, za unyizi, za bo bo bo si za bho bho
Ukaphophonya, fufuta
Yambiranso koma uzindikile mbali ina ya moyo uyimisa
Ndi struggle yobereka ukakanika kupilira
Kumasewero'wa lowa theater, Do chi ceasar.
Ma resources ndikuthula
Koma ukadya uchi usanawete njuchi ndikufula
Ntolo wako ukakulemeletsa ndikutula
Ukalowetsa Chibwana mmoyo wako nkutuluka
Poti Iwe ndi odontha; chi bekete
Tchera khutu ugwire mau usayang'ane mphepete
Ma pain onse aja purpose yako suinapezebe
Zitsotso zonyansitsa moyo wako sunasesebe
Mbeu sunafesebe, ndime sunagwetsebe
Moto chikupatsile mpaka pano sunabebebe
Ukumangowinya ma excuse ngati ka baby be
Nkana sukuwina mmanja mwako muli mbe mbe mbe
Ubwenzi ndi wachikondi wokuzunza sunathetsebe
Khoma la banja la ukapolo sunagwetsebe
Maso sunapenyebe
Zoti Matafale anati ukamadya usadziyese ndiwe mfulu sunamvetsebe
Matcheni sunabreakebe, ntanda sunansenzebe
Plan sunalembebe, Mimba sunaphwetsebe
Kumangokamba za anthu ndi zinthu ngati Zebede
Anzako nzawo zikapsya iwe nsanje ngati Gwenembe
Khomo la ufulu...lili pa ntetete
Atsogoleli akhungu akumakulozela pa mphepete
Wasanduka chidempete
Ntengo wa moyo wako wonse lero watsika wafika nde nde nde ndi njenjete
Tiye menya pelete
Usayimike phazi mpaka ntendere upezeke ufulu ukuchengete
Written by: Pilirani Kumasewera